Psalms 60

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.

1Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.
Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
2Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,
konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
3Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;
inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.

4Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera
kuti tisonkhanireko pothawa uta.

5Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja,
kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
6Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
“Mwakupambana ndidzagawa Sekemu
ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
7Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
8Mowabu ndi mbale yanga yosambira,
pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga,
pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”

9Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa?
Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife
ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu,
pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano
ndipo tidzapondaponda adani athu.
Copyright information for NyaCCL